Baibulo labwino zedi, lokhala ndi zithunzi zoonetsa zimene zikuchitika, tsopano latanthauzidwa m’chinenero chanu:
Nsembe. Nkhondo. Mayesero. Chiwembu. Chiyembekezo. Chipulumutso.
Mulungu anasankha kudzivumbulutsa yekha kwa anthu, osati kudzera mu mfundo zokhazikika chabe, kapena m’nzeru chabe, kapenanso m’ziphunzitso chabe, koma makamaka kudzera m’nkhani za uneneri, nkhondo, chifundo, chiweruzo, zozizwitsa, imfa, moyo, ndi chikhululukiro.
Nkhani ya mmene Mulungu anakonzera kupulumutsa anthu yafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera m’buku la Genesis mpaka Chivumbulutso. Iwo amene adaonapo mmene buku la Marvel Comic lidalembedwera, akukondwera kwambiri ndi ntchito yopatsa chidwi imene ili m’buku la Zabwino ndi Zoipa. Zithunzi zake ndi zapamwamba kwambiri komanso zopatsa chidwi.
Inde, Baibulo lotchuka zedi, lokhala ndi zithunzi, lotchedwa Zabwino ndi Zoipa, latanthauzidwa tsopano m’chinenero chanu! Buku limeneli limakuthandizani kudziwa mwatsatenetsatane nkhani yonse ya m’Baibulo mosavuta. Limaonetsa nkhani zikukuzikulu m’njira yosavuta kutsatira yonga ngati sewero. Pansi pa tsamba lililonse pali kalozera wa m’Buku Lopatulika kuti inu owerenga muthe kuwerenga nkhani yonsewo m’Baibulo. Bulu lapamwambali, lolembedwa ngati sewero, lili ndi masamba 320 okhala ndi nkhani za m’Baibulo.
Binding | Perfect Paperback |
---|---|
Pages | 320 |
Media | |
Subtitle | (Print-On-Demand, Shipped Separately) |
Language | Chichewa |
Author | Michael Pearl |